Winners chapel International Balaka

Winners chapel International Balaka

Share

.

02/05/2022

*USAYEREKEDZE KUCHITA ZOMWE UKUGANIZAZO, UDZALIRA!!!!!!!! *
________________👇________________

-Ndiwe bambo Uli ndi chuma chambirimbiri ndipo Uli pa banja, poti zikukuyendera ikuganiza zotenga mitala😢 ndikukuudza pano kuti ukango yerekedza KUCHITA zomwe ukuganizazo, udzalira ndithu. Chuma chomwe ukuchinyadiracho ndi mabizinesi akuyendawo, adzasokonekera, chuma chako chidzatha. Kafuse anzako adzakuudza,,,, ( mudalitso wa Mulungu suyanjana ndi nyasi)

_winawe zakuthina , bizinesi siyikuyenda kuyesa umu ndi umu ndalama osayiona. Pano ukuganiza zokalowa satanic, mmmmh, ukadzango joyina udzapalamula mabvuto oposa omwe ukuwaonawo. Kafuse anzako akakuuza, ndikunena pano wina wake akulira😭😭😭, kuti akadaziwa sakada panga mistake yo joina.

-wakopeka ndi anthu achuma, ndipo wafutsafutsa kwa anzako, iwo akulozera kwa sing'anga wotchuka kudera lanulo, koma ine ndingokusina khutu kunena kuti, ukangoyerekeza KUCHITA zomwe ukufunazo ukhala wotembereredwa!!! Mesa ndiwe mtumiki iwe, kodi sindiwe MUKHRISTU iwe??? Nanga bwanji ukusiya sing'anga wamkulu YESU KHRISTU, kutsata ziwanda?? Udzalira ndithu!

-Ndiwe mzimayi, m"banja lanu mumangokhalira kukangana, koma utamvetsedwa ndi ankako kuti kuli mankhwala ochikuda, ompanga mwamuna wako kuti adzikumvera ndi kukukonda. Koma pano ndikuudze, kunena kuti ukadzayerekedza kuchita zomwe ukuganizazo. Banja lako lidzatheratu.

-MUKHRISTU siwotsatira zozizwa, koma kupanga zozizwa(Yohane 14:12) ukapitiriza kuyenda yenda mwa azitumiki kufuna zozizwa, udzathera konko.

-Ndiwe m'nyamata , ngakhale ndiwe wokhulupirira, koma wakhala ukugwa chifukwa cha zilakolako za thupi . Ndipo mpakana waganiza zongosiya kupemphera. Koma ndikukulimbikitsa lero kuti usafooke, popeza Yesu Khristu anatilimbikitsa kuti TIYETSETSE KULOMA PAKHOMO LOPAPATIZA(LK 13:24) indedi ukuyenera kuyetsetsabe, kukangamirabe. MULUNGU sanakutaye!

ABALE PA CHISANKHO CHILICHONSE M'MOYO UNO, TIKUYENERA KUSANKHA MWA NZERU KUKANA KULIRA PA MAWA.

"Yetsani zonse; sungani chokomacho"
(1Atesalonika 5:21)

Pangani like page yathuyi kuti mudzirandira nao mauthenga ena ndikupanganso share uthengau mumagulupu onse a pa Facebook.

Utthenga Wachitsiriziro page

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Balaka?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address

Balaka
Balaka