Nkhani Za M'maboma

Nkhani Za M'maboma

Share

🌍THIS IS THE LATEST & FASTEST GROWING PAGE FOR BREAKING NEWS🌏 . Welcome 😎kuing'alura osaopa😎💪💪

Photos from Nkhani Za M'maboma's post 24/08/2026

Kalikonse Tikaona

Mtsogoleri wa kale wa dziko lino, a Lazarus Chakwera wati aMalawi atengere chitsanzo pa mavuto omwe akukumana nawo pakadali pano ndi kulingalira mozama.

A Chakwera ati anthu asalole kuti agonjere kumavuto omwe akukumana nawo m'dziko lino, koma kuti adzuke ndikuyang'ana chitsogolo.

Iwo ayankhula izi lero pasitolo zapa Mponela ku Dowa, pomwe anayima pa ulendo wawo wochokera ku Kasungu, komwe anali nawo pa msonkhano wawukulu wa mpingo wa CCAP Synod of Livingstonia.

A Chakwera omwenso ndi mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress (MCP) anapereka chitsanzo cha ulimi wa fodya, womwe ati amvetsedwa kuti alimi ambiri sanagulitsebe fodya wawo, komanso ena aberedwa ku msika.

Phungu wanyumba ya malamulo m'dera la pakati kwa boma la Dowa, a Annie Chibwana anayamikira a Chakwera, kaamba kovomera kuyima kwa nthawi yochepa kuti ayankhule ndi anthu otsatira chipani cha MCP m'derali.

(by Wilson Henry

19/08/2026

Tamvani

Mai wina wa zaka 28, a Atness Thom wacheka kumalo obisika mai nzake atamupeza akugonana ndi mamuna wake ku munda m'dera la Kapichi ku Monkey Bay.

Malingana ndi mneneri wapolisi ya Monkey Bay, a Kondwani James, maiyu anapezelera mai nzakeyu, a Doreen Witness, azaka 21 akugonana ndi mamuna wake m'munda wina, usiku wa Lolemba.

"Atawapeza awiriwa akugonana, maiyu anayamba kulimbana ndi mai nzakeyu ndipo potengera kuti mai ovulazidwayu anali osavala, maiyu anamucheka nzakeyu kumaliseche," atero a James.

Mneneri wa polisoyu wati pakadali pano, maiyu amutengera ku bwalo la milandu, pamene mai ovulazidwayu anamutengera kuchipatala cha Monkey Bay komwe anakamusoka mabala.

(by Alex Batison -Monkey Bay:08/19/26)

18/08/2026

🇿🇲 BREAKING: PRESIDENT HAKAINDE HICHILEMA WINS SECOND TERM IN ZAMBIA

President Hakainde Hichilema has been re-elected for a second five-year term, securing about 61% of the vote. His main challenger, Brian Mundubile, polled about 38%.

The next five years must be about:
🔹 National reconciliation and healing
🔹 Respect for democratic institutions and the opposition
🔹 Jobs, investment and inclusive growth
🔹 Easing the cost of living
🔹 Stronger national unity

Winning gives a leader a mandate. Reconciling a nation gives that mandate legitimacy.

The election is over. Now Zambia must unite, reconcile and build.

Congratulations to the people of Zambia for a peaceful democratic exercise.

🌍 Transtropics MegaChoice
Building Ideas, Inspiring Africa

18/08/2026

Good Morning 🏵️🙏

11/08/2026

Good morning

Photos from Nkhani Za M'maboma's post 08/08/2026

MALAWI WALUZA MUNTHU OFUNIKIRA😭😭

A Naomi Banda, amene ndi mchemwali wawo wa malemu Brian Banda, ati Brian anayamba kudandaula vuto la kusanza kumayambiliro a sabatayi.

“Kenako titapita nawo ku chipatala ndi pamene anawapeza ndi malungo. Koma dzulo atadya chakudya cha madzulo anafooka kwambiri ndipo tinathamanga nawo ku chipatala kumene amwalira mmawa wa lero," iwo atero.

Pakadali pano, tsiku loyika m'manda malemuwa, amene anali woyamba kubadwa m'banja la ana asanu ndi atatu, silinadziwike.

Akubanja ati siwa ikachitikira kumudzi kwawo ku Chileka m'boma la Blantyre.
Malemu Brian Banda anabadwa m'chaka cha 1981.

Wolemba Isaac Salima

Photos from Nkhani Za M'maboma's post 02/08/2026

FULL-TIME

Egypt 🇪🇬 1-3 🇲🇼 Malawi
Iman Hassan 71' Rose Kadzere 35'
Faith Chinzimu 45+2'
Temwa Chawinga 68'

2/2 ✅
6pts ✅
Top of the group

01/08/2026

Kusuta bositiki, m'buka kwakula kwa Chemusa

Pali chiopsezo kuti chiwerengero cha achinyamata ozungilira mitu chitha kukwera kwambiri kudera la Chemusa munzinda wa Blantyre komwe akuti mchitidwe osuta bositiki omatira zinthu komaso miyala ya m'buka wafika posauzana.

Fred Msiyambiri yemwe ndi khansala wa wadi ya Mussa-Magasa anadandaula zakukula kwa mchitidwewu pa maliro ena mderali Lachitatu sabata ino, komwe anachonderera achinyamata kuti asiye.

…Msiyambiri wati achinyamatawa akasuta m'buka kapena bositiki, akumatha masiku atatu osamva njala komaso osagona tulo, ndipo watiso masiku atatu akatha, bositikiyu akayamba kusungunuka m’mutumo, osutawo akumathaso masiku ena atatu osamva njala komaso osagona.
..Malingana ndi Msiyambiri, achinyamatawa akumaika miyala ya m'buka mu babu lomwe akumalilumikiza ndi payipi ya cholembera, kuyatsa ndikumasuta. Mbali inayi, bositiki akuti akumamuika mujumbo, kumukhutchumula kenaka ndikumafwenkha mpweya wakewo.

29/07/2026

Malawi 3
Nigeria 2
⚽🇲🇼🇲🇼
WAFCON

27/07/2026

Vuto la mayendedwe kwa anthu okhala m'mudzi mwa Mkwete, mfumu yaikulu Nthache m’boma la Mwanza likhala mbiri ya makedzana tsopano kutsatira mlatho wamakono omwe wamangwidwa ndi wochita malonda wina, a Gracewell Mapande.

Poyankhula ndi Zodiak Online atatsegulira mlathowu, a Mapande ati iwo siandale koma achita izi pofuna kuchepetsa mavuto omwe anthu okhala m'derali akhala akukumana nawo.

A Mapande ati akukhulupilira kuti mlathowu uthandizanso kutsegula khomo la ntchito za malonda ndi chitukuko m'derali.

Ndipo, wapampando wa khonsolo ya Mwanza a Kaisi Chimbalanga wayamikira a Mapande kaamba ka chitukukochi chomwe ati chithandiza kutukula ntchito za mtengatenga ndi mayendedwe m'derali.

M'modzi mwa anthu okhala m'derali, a Frank Gomani wati ndiokondwa ndi kubwera kwa mlathowu womwe ati uthandiza kuti ntchito za chitukuko zomwe zimalephera kufika m'mudzimo monga mijigo ndi zina ziyambe kubwera tsopano.

(by Greenwell Kayuni - Mwanza:

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Website

Address

Lilongwe
INVITESOTHERSTOLIKETHISPAGEOF