Frank POG Nsewa

Frank POG Nsewa

Share

Supporter Wazoona

16/05/2026

Mkazi ochita zisudzo za akaluakulu Mary Rock walonjeza otseka pagolo wa timu ya PSG Matvey Safonov kuti ngati sakachinyitsa chigoli mu mndime yotsiliza ya mpikisano wa UCL akamupatsa chakudya chokoma kwambiri chimene sanachitchule.

Mary walemba uthengau pa Instagram ngakhale mkazi wa otseka pagoloyi sizinamusangalatse koma Safonov sanaikepo mulomo.

16/05/2026

Match day

15/05/2026

Azaumoyo muzinda wa Toronto ku Canada alengeza kuti anthu onse amene apite kumeneku kukaonera mpikisano wa FIFA World Cup 2026 azikalandira ma condom aulere.

Iwowa akuti anthu sakaononga ndalama zawo zina kufuna kupewa matenda opatsilana pogonana kapena mimba.

USA, Canada komaso Mexico ndi maiko atatu amene kukachitikire mpikisano wa FIFA World Cup 2026 koma chifukwa cha fundo iyiyi anthu ambiri akaonelera ku Canada.

11/05/2026

Zamu week 4 🔥🔥🔥

10/05/2026

Dzulo mphunzitsi wa timu ya PSG Luis Enrique wayankha chifukwa chimene otseka pagolo wake Safonov goal kick yake amatulutsa komaso amamenyera mbali imodzi nthawi imene timuyi imakumana ndi Bayern Munich.

Enrique akuti style yotere anaitenga kumasewelo aja a rugby ndipo cholinga chimakhala chofuna kuti osewela azidzadzana mbali imodzi imene kukupita mpirayo kotelo timu inayo simapanga attack kwambiri mbali yomwe kukutulukila mpirayo chifukwa kumakhala gulu.

Iyeyu anadziwa kuti mbali imene kunali osewela wa Bayern Michael Olise ndiye yoopsa ndiye anauza otseka pagolo wake kuti azitulutsila kumeneko kuti kukhale chinamtindi cha osewela kotelo Olise sayenda chifukwa omupanga block achuluka.

09/05/2026

Yanu ndi iti?

08/05/2026

FIFA yatulutsa masiku amene ma timu a maiko omwe akupita ku mpikisano wa FIFA World Cup 2026 atulutsile maina a osewela amene apite kukatumikila ma timuwa.

08/05/2026

Bibida ndi mafanta a m'botolo la grass sizololedwa ku mpira.

Super League of Malawi (SULOM) labwereza kukumbutsa mbali zonse zokhudzidwa kuti pa masewero a mpikisano wa FDH Bank Premiership sikuloledwa kugulitsa zakumwa zomwe zili m’mabotolo a galasi, kuphatikizapo zakumwa zoledzeretsa, mkati kapena mozungulira bwalo la masewero.

SULOM yatinso kulowa kwaulere (malova) sikudzaloledwa m’mphindi zomaliza za masewero aliwonse a FDH Bank Premiership.

08/05/2026

Moses Chavula wasankhidwa kuti atsogolere Ekhaya FC pambuyo pakuyimitsidwa ntchito kwa mphunzitsi Enos Chatama chifukwa chosayamba bwino season ino nditeamuyi

Chavula si wachilendo ku Ekhaya FC chifukwa anaphunzitsapo timuyi mu Southern Region Football Association Premier League ndipo anathandiza kuti ipangidwe promote mu Super League.

Welcome Chavula ichichi aphwanga muphwetekedwa samalani
Frank POG Nsewa

Photos from Frank POG Nsewa's post 06/05/2026

Mwana wamkazi wa Victor Osimhen, Hailey Osimhen, ndi mmodzi mwama supporter ake akuluakulu omwe amamuthandiza kwambiri. Nthawi zambiri samaphonya masewera apa home a Galatasaray, ndipo amaoneka nthawi zambiri ali kuma stand akusapotela abambo ake ndi mtima wonse.

Atatha masewera, pali chizolowezi chosangalatsa: Osimhen amatenga Hailey kupita naye m'bwalo, kumene amayenda limodzi akupeleka moni kwama supporter powaweva.

Nthawi zambiri amakhala limodzi pa zikondwerero za Galatasaray pambuyo pa masewera, kugawana chisangalalochi ndima supporter ,zomwe zimakulitsa ubale pakati pa wosewera, banja lake, ndi club yake.

Nthawi zimenezi ndi zofunika kwambiri kwa Hailey ndi Victor Osimhen.

Pakali pano, mwina Hailey sakuzindikira bwino zimene abambo ake akuchita kapena kuti bambo ake ndi player wamkulu mu mpira. Iye akadali mwana, akungosangalala kukhala pafupi ndi abambo ake, kumva phokoso lama supporter ndi kumva mmene zinthu zilili pa masewera a Galatasaray. Koma tsiku lina, akadzakhala wamkulu, adzamvetsa zonse bwinobwino.

Adzasunga nthawi zimenezi mu mtima wake nthawi zonse—nthawi zimene abambo ake ankamutengera ku stadium, chisangalalo chomaona akusewera, komanso kuyima naye pambuyo pa masewera kuthokoza ma supporter.

Kwa Osimhen, izi ndi zokumbukira zomwe sadzaiwala. Mpira udzamupatsa zigoli, makapu, ndi kupambana kwakukulu, koma nthawi ngati izi ndi mwana wake ndi zosiyana kwambiri.

Akadzayang’ana zithunzi ndi makanema a masiku ake osewera, sizidzangokhala za mpira yokha, koma za ubale wake ndi mwana wake, kuseka kwawo, ndi zokumbukira zomwe adapanga limodzi pa bwalo.

05/05/2026

Masewero a timu ya Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets asunthidwa kuchoka pa 14:30hrs kufika pa 16:30hrs.

Bungwe la Super League of Malawi ndi lomwe lalengeza za nkhaniyi lachiwiri masana.

Bungweli lapanga ganizoli pofuna kupereka mpata kwa masewero a Blue Eagles ndi Silver Strikers omwe adzakhale pa bwalo la Civo lamulungu lomweli.

Matimu a Wanderers ndi Bullets adzakumana pa bwalo la Bingu lamulungu mu mzinda wa Lilongwe kutsatira kuti bwalo la Kamuzu ndi lotsekedwa.

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Lumbadzi?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Website

Address

Lumbadzi Post Office Box 44
Lumbadzi