Stellah's short stories

Stellah's short stories

Share

this page is for only entertainment

07/05/2022

Funny ppl

02/05/2022

πŸ”₯βœ”

29/09/2021

*_Grand P* { *Moussa Sandiana Kaba}*
_
_Star Warelo_ ✍️

Lero tiyeni tiwerenge History ya m'modzi mwa anthu odziwika muno mu Africa--- maka maka ku west Africa ndikunenatu za _Grand P ._

✍️_Grand P_ ili ndi dzina lomwe amadziwika nalo lodyela, koma iye dzina lake lobadwa nalo ndi { *Moussa Sandiana Kaba}* Grand P anabadwa pa 13 October 1993-- adabadwila ku dera lomwe limatchedwa Sanguiana Nabaya mu dziko la kwawo ku Guinea (pa chaka cha kubadwa apo ena amati ndi 1990 koma mukufufuza kwa ine ndapeza malo ambiri palembedwa 1993) , *Grand P* pakanali pano amapatsidwa ulemu mu Africa ngati m'sangalatsi kamba ka nyimbo zake zosangalatsa . *Grand P* atabadwa ma dokotala adadzamupeza ndi matenda pa chingelezo matenda awa amatchedwa ( progeria) matenda awa amapangitsa k*ti munthu thupi lake lizioneka okalamba ngakhale ali mwana, komaso thupi limakula lonyentchela & mau amaveka ngati kamwana. Grand P ali wa chichepele ati palipose pomwe an'kayenda amakhala akusekedwa ndi ana azizake ngakhaleso anthu akulu akulu, koma iye sadafooketsedwe ndi kusekedwa komwe ena an'kamuseka. *Grand P* luso lake loyimba lidaonekela atatulutsa ka video clip komwe adayimba nyimbo yofunila mafuno abwino team yokankha chikopa { *_Guinea Football National Team}_* ndipo Africa Cup of Nations yomwe idapangidwa host ndi dziko la Egypt mu chaka cha 2019 Grand P adaitanidwa kumeneku kukasangalatsa anthu , Grand P wakhala akunena monenetsa k*ti sadzatengela style kapena k*ti mayimbidwe a wina aliyese iye adzafa ndi mayimbidwe ake ake. Grand P poyankhapo za anthu omwe amamuseka maonekedwe ake wakhala akuyankha poyela k*ti (poti Mulungu adamulenga choncho--- icho ndi chifunilo cha Mulungu-- komanso kamba ka matenda omwe adabadwa nawo palibe chomwe iye angapange) Grand P amapitiliza kunena k*ti akudziwa zoti pali anthu omwe amamukonda ngakhale maonekedwe ake ali onyentchela, and adati amadziwa zoti pali anthu ena amaseka maonekedwe ake omwe iye sadachite kufuna amamaliza ndi mau oti { _such is life you can please everbody}_ --- ali wa m'ng'ono Grand p ak*ti san'kadziwa m'komwe k*ti tsiku lina adzakwela ndege koma pakanali pano iye ndege amakwela momwe wafunila, atangoyamba kufuna kukhala oyimba Grand P adathandizidwapo ndi anthu omwe amasangalala ndi nyimbo zake ena mwa iwo m'kukhala anthu a ndale monga a *Baidy Aribot* akulu awa ndi Vice governor of central Bank of Guinea ndi omwe adapanga dongosolo loti Grand P akwele ndege ulendo okasapota team ya m'pila wa mwendo ya dziko la Guinea ku African Cup Finals omwe udachitikila ku Egypt--- atachoka ku Egypt adaitanitsidwa ku Mali komwe adakakumana ndi anthu omwe ali ndi matenda ofanana ndi omwe Grand P adabadwa nawo, izi zidapangitsa k*ti ambiri anthu ku dera loyandikana ndi dziko la Guinea ayambe ku mukonda Grand P-- olemba news paper adadzamutcha Grand P k*ti ndi New ambassador of the good dedicated .

_Star Warelo --_ ✍️

Pa ulendo wake omwe adali ku Mali Grand P adapemphedwapo kuimba ndi oyimba otchuka wa ku Mali *(Oumou Sangare--- Sidiki Diabate)* komaso adaitanidwapo ndi kukakumana ndi Saidou Keita mwana wa president --- Grand P sadasiile pompo adakafikaso ku Ivory coast komwe adakaimba ndi DJ Arafat , El Poueblo Bravador ndi ena ambiri oyimba odziwika ku Ivory coast, momwe an'kayenda mu maiko onsewa amayenda namakumanaso ndi anthu omwe adabadwa ndi nthenda yofanana ndi yomwe iye Grand P adabadwa nayo monga Ambassador for short people. Grand P kumbali ya chikondi ali pa ubwezi ndi m'tsikana wa ku Ivory coast dzina lake *Eudoxie* m'tsikana uyu amadziwika ndi dzina lodzichemelela loti Kim Kardashian of Africa , ku maiko a ku West Africa Eudoxie amawelengedwa k*ti ndi yemwe ali ndi matako *(mbina kapena k*ti chinyophilo)* kuposa akazi ose a ku west Africa, Grand P adafusila Eudoxie mu August 2020 ndipo adati pali chiyembekezo choti adzamangitsa banja lawo mu 2021, koma ambiri anthu akhala akunena k*ti Eudoxie adavomela Grand P pongofuna ndalama osati chikondi koma m'tsikanayu wakhala ak*tsutsa izi k*ti ndi sanje chabe za anthu. Pa live show yomwe idakozedwa ndi a Kerfalla Kante mu 2019 ku Conakry peoples place a Grand P adakaikilidwa ndi anthu ambiri zoti angakwanitse kuimba pa Stage komatu Grand p adaimba pa show iyi posalingalila za matenda kapena maonekedwe ake, osaiwala monga ndafotokoza pamwambapo k*ti adali m'modzi mwa ma delegates omwe adapita ku Egypt ndi team ya Guinea ku Africa Cup of Nations izi zidapangitsa kwambiri k*ti Grand P ayambe kukondedwa ndi anthu ambiri mu Africa ndi maiko a ku Ulaya--- monga ndafotokozapo pamwambapo k*ti Grand P waimbapo ndi oyimba odziwika ku Guinea adaimbaposo ndi Azaya, King Alasko ma collaborations oterewa adapititsa mbiri ya Grand P patali--- Grand P ali ndi Album yotchedwa (title) I *Khadi nanna"* ndi ma single angapo monga " *Grand P Barana" Life" Syli"* mu 2019 adapangidwa feature ndi Sidiki Diabate single " *Irhafama* " pa 11 September 2020 adapangidwa feature ndi Boncena mu single title " *Amour Ndoto* ".

*_Star Warelo*_

Grand P ndi m'modzi mwa oyimba olemela (rich) ku Guinea pali chiyembekezo choti ali ndi ndalama zosachepela $10 million US dollar, Grand P eya ndi oyimba komasotu amapanga nawo za ndale (politics) Grand P adalengeza k*ti apikisana nawo pa zisankho zomwe zidachitika mu dziko la Guinea mu 2020 mwezi wa October zisankho izi adawina ndi a { *Alpha Conde}* term ya number 3 koma ambiri adati a Alpha Conde adabela zisankho izi # tiyeni tikumbukile k*ti a Alpha Conde adalandidwa boma ndi asilikali masabata angapo adutsawa. A Grand P popanga ubwezi ndi m'tsikana wa ku Ivory coast (Eudoxie Yao) zidawapangitsa kukhalaso ndi fun base yaikulu mu dziko la Ivory coast. Pa kufuna kupikisana nawo kwa bwezi lake Eudoxie adati amuna ake omwe ndi president wa m'tsogolo muno wa dziko la Guinea, adafuna k*ti naye ayimile u president pa zisankho za mu Ivory coast ndi thandizo la ndalama zopatsidwa ndi bwezi lake Grand P zitamuvuta iye adati ngakhale zamuvuta ku Ivory coast iye Eudoxie ali ndi chikhulupilo choti one day adzatchedwa first lady wa dziko la Guinea

✍️
Ndimalize motere *(Grand P)* ndi nick name-- kapena k*ti dzina lodyela πŸ‘-- dzina lobadwa nalo ndi { *Moussa Sandiana Kaba}*

✍️Kwawo ndi ku { *Guinea* } --- Fiance kapena k*ti bwezi lake ndi *(Eudoxie Yao)* wa ku Ivory coast.

✍️ Mu 2020 adasaina contract ndi ma company a ku America awiri omwe amamupanga sponser.

✍️ Za family yake komanso momwe adakulila ku ubwana ndi maphuzilo ake sindidathe kupeza information yotereyi.

✍️(Progeria) awa ndi matenda omwe *Grand P* adabadwa nawo, matenda awa munthu amayamba kukalamba maonekedwe ali wang'ono, munthu amatalika kufika pa 1 meter osadutsa, pa scale amakwela 25 kilograms osadutsa.

✍️ mu 2020 *Grand P* adali olemela $10 million US dollar, pali chiyembekezo choti pofika mu 2021 ali ndalama zodutsa $12 million US dollar--- Grand P ali ndi nyumba ya pamwamba kwambiri ( mansion) ili mu m'zinda wa (Conakly) ku Guinea ndipo ndi m'modzi mwa oyimba ( musicians) olemela muno mu Africa πŸ‘ Grand P ali ndi ma galimoto a pamwamba monga Lamborghini, Masserati ndi zina zotelo.

✍️ *Grand P* ndi member wa chipani chotchedwa (ACU) ndipo ali ndi chikhulupilo k*ti adzawina ma primaries ndi kuimila chipanichi pa zisankho za 2025.

Ndateremu ine ndakwangula kufotokoza mbiri ya Grand P monga mwa pempho lanu ma Star

πŸ‘ Mu comment box nenani k*ti next or Dzimele

; Nkhaniyi yachita kumatulidwa kuchokela ku group lathu lolipilisa la Star Walero family, ndi K300/R15 pamwezi, mukationa zii pano tikumakhala kumeneku and nkhan zambiri zikumavumbulukaso kumeneko. Tipezen ku inbox or pa Whatsapp
+265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 & +27 71 099 2089 k*ti mujoine lero!

@ *Dzufunadzimelendevuidzidzi*

Photos 06/09/2021

ADAMS WATISIYA ATAKOMOKA KWA ZAKA 39

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo m'dziko la France lalengeza k*ti katswiri wawo, Jean-Pierre Adams yemwe anakomoka zaka 39 zapitazo wamwalira lero chakum'mawaku kuchipatala chotchedwa Nimes University Hospital.

Jean-Pierre Adams, yemwe anabadwira mumzinda wa Dakar m'dziko la Senegal, anakomoka mwezi wa March m'chaka cha 1982 madotolo atalakwitsa magwiridwe a ntchito awo pamene amamupanga opaleshoni ya pa bondo.

Katswiriyu, yemwe wasewelerapo timu ya France m'masewero opitilira makumi awiri, wamwalira ali ndi zaka 73 ndipo wasewelerapo matimu monga Nimes, PSG komanso Nice.

Chikomokeleni osewerayu, France yatengapo zikho ziwiri zampikisano wa padziko lonse pachingerezi World Cup; koyamba mu 1998 kenako mu 2018.

20/08/2021

*DID YOU KNOW*...?..
1. Pa anthu 100 alionse, ndi anthu awiri okha mungawapeze ndi maso a green.
2. Agalu nthawi zina amalenga ngat adwala cholinga kungofuna attention ya amene amayang'anila
3. Mphevu nkachinyama komwe kamanyasidwa kwambiri munthu ukakagwira, kungokagwra or kukagunda kamathamanga pompopompo kukazisuka thupi lonse...
Star Walero family ..
4. Ku England kuli mtsikana kamwana kenakake kotchedwa Olivia Farnsworth, iyeyi anabadwa ndi ma chromosome odabwisa kwambiri nthupi mwake (Chromosome 6 Deletion) samva njara, samva kupweteka and satopa k*ti akufuna kugona. Mu 2016 anagundidwa ndi galimoto kwambiri anthu kuona choncho koma sanavulale kwambiri and sanamveso kupweteka, ndipo ma doctor anampasa nickname ya "Bionic girl"..Amachit kufuna ekha k*ti adye not k*ti wamva njala, and kugona not k*t watopa.

5. Mtima wa Blue whale (chinsomba chachikulu umalemela 600Kg)
6. Mtundu weniweni wa dzuwa si Yellow koma white.
7. Ku Norway kuli church dzinalake Stave Church, chinamangidwa zaka 800 zapitazo opanda nsomali, mitengo basi koma sichinagwepo and ncholimbabe pano.



8. Jamaica flag ndi flag yokhayo padziko lapansi imene ilibe mtundu wa red, blue or white pa mbendela yake.
9. Basenji ndi galu yekhayo amene samatha kuhuwa, sahuwa ngat agaluwa enawa akafuna kuluma amangoluma mwa silent and akamathamangisa munthu sahuwa ndati.
10. Munthu kungopezeka wapha Njovu ku Sri Lanka umaphedwa siku lomwelo..
```KODI MUKUDZIWA??```
Ma facts onsewa akubwera chifukwa cha group yathu yolipilisa ya Star Walero family, ndkumene kumavumbuluka nkhani zambiri and zambiri zimayamba kuponyedwa kumeneko zisanafike pano..Ndi K300/R15 pamwezi. Tipezeni pa; +265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 and +27 71 099 2089 k*ti mulowe ku family...
Phosomthumba sanatope ndikupitilizabeπŸ‘‡πŸ½πŸ‘‡πŸ½πŸ‘‡πŸ½..
11. Plover bird ndi mbalame yokhayo imene imatha kukhala mkamwa mwa ng'ona koma osadyedwa. Chinsinsi chake ndichak*t imachosa nyama yokanilira mmano mwang'ona iyo kumadya, ndipo ng'ona imakondwela

12. Australian Bussinessman komanso Blue Star line company, Clive Parmer, Wati akupangaso Titanic ship ndipo iyi ikhala Titanic 2.0. Palmer analengeza izi mu 2018 k*t by 2022 stimayi izakhala itayamba kuyenda, Titanic 2.0 ati ikhala yayikulu and yabwnoso kwambiri ngati yoyamba ija ndipo izinyamula anthu 2435, ndalama zomwe zalowa kupangla sitimayi ndi $500M

13. Ku Australia kuliso mzinda omwe uli pansi padziko otchedwa "cobber pady".. Mu 1915 kumkatentha kwambiri ku Australia mpaka temperature ya 50 degrees ndipo anthu anayamba kuganiza k*t bwanj titamakumba pansipa tizikhala ndipamene anayamba kupanga, mpaka pano ndi City yomwe ili pansi pomwe timapondapa. Kuli Manyumba, church, misika ndi ma hotel.
14. Indonesia ndi dziko limene kuli anthu afupi ambiri padziko lonse lapansi

15. Ku California, America kuli bulb yotchedwa Centennial yomwe inayamba kuyaka 1901 mpaka pano sinathimebe or kupsa. Ndi bulb lokhalo padziko lapansi lomwe lakhala zaka zambiri osapsa.

16. Nkhono (snail) imatha kugona kwazaka 3 osazuka inu kumati inafa koma ikugona.
17. Mkadzi wa Feoddor Vassiilyev (1707-1782) ndi mzimayi yekhayo amene anabeleka ana ambiri pakamozi (69). Ma twins ma pair 16, Ma triplets ma set 7 komanso ma set a ma Quadraplets 4. Atabeleka pompo, anamwalira...
Mwawerenga mwamaliza etii??😁😁 Sopano Pangani SHARE mma group omwe muli amzanu ena awerenge...
😊πŸ’₯😁.
; Nkhaniyi yachita kumatulidwa kuchokela ku group lathu lolipilisa la Star Walero family, ndi K300/R15 pamwezi, mukationa zii pano tikumakhala kumeneku and nkhan zambiri
zikumavumbulukaso kumeneko. Tipezen ku inbox or pa Whatsapp; +265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 & +27 71 099 2089 k*ti mujoine lero!

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address


83 Mayani Dz
Lilongwe
MW