Madyedwe A Machiritso

Madyedwe A Machiritso

Share

Chakudya chanu nthawi zonse chizikhala mankhwala ndipo mankhwala anu odalirika azikhala chakudya!

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

NDIWO ZA MASAMBA A MPINIMBI
✓Ndikudziwa kuti izi ndi zachilendo mwina ambiri simukudziwa kuti masamba a mpinimbi amakhoza kuphikidwa ndipo mukhoza kudyera nsima kapena mphunga.
✓Anthu a ku Nigeria amaphika ndipo amasakaniza ndi zakudya zina.
✓Ngati mtengowu simukudziwa chonde musayerekeze kutenga masamba ndi kuphika ngati ndiwo kuopa kuti mungagwiritse ntchito mtengo omwe sindiwo.
✓Masamba amene amafunikira ndi ophukira kumene osati okhwima. Mwina ndinene kuti a nkhanda.
✓Masambawo amawawira pang'ono koma vutolo limathetsedwa potsira nsinjiro, tomato, anyezi ndi mchere.
✓Poyamba mumatenga masamba athlete kapena ankhanda a mtengo wa mpinimbi ndi kuwatsuka bwino; penanso ndi madzi otentha.
✓Kenako phikani masambawo monga muchitira ndi ndiwo zina za masamba.
✓Kenako tsirani nsinjiro, tomato, anyezi ndi mchere ndipo takasani.
✓Dikirani pang'ono ndipo kenako mukhoza kuphula.

✓Mukhoza kudyera nsima kapena mpunga.
✓Ziri ndi ma vitamins monga vitamin A, C komanso michere monga Calcium, iron, Copper ndi magnesium.
✓Ndizothandiza kwa anthu omwe ali ndi mavuto a mmimba, anthu amene BP ndi yokwera, anthu ochepekedwa magazi, komanso anthu amene ali ndi mavuto okhudzana ndi kuphwanya kwa thupi. Ndiwozi zimatha kuziziritsa ululu.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

MPINIMBI
✓Ndiyetu zipatso zimenezi ziri ndi mlingo wabwino wa Omega-3 fatty acids komanso Omega-6 fatty acids.
✓Awati ndi mafuta abwino zedi amene amathandiza thanzi labwino la mtima, ubongo, m'mitsempha ya magazi komanso chiwindi.
✓Kuonjenzera apo zipatsozi ziri ndi mlingo waukuru wa fiber. Choncho ndi zothandiza kuonjenzera thanzi labwino la chifu komanso matumbo akuru. Zimathandiza kuti chiwerengero cha ma bacteria abwino m'thumbo lalikuru chikwere zomwe ndi zothandiza kuteteza matenda osiyana siyana kuphatikizapo matenda a shuga.

Ife a Eden Green Nursery and Food Forests kuno ku Ntcheu tikhala tikukupatsirani zambiri zokhudzana ndi Mpinimbi, Mahuhu ndipo ena akuti Mtonongoli.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

MALABAR CHEST NUTS
✓Mawa wa lero ndalandira parcel imeneyi kuchokera kwa mmodzi otsatira tsamba lino wa ku Mchinji.
✓Iye, zaka zambuyomu anagula mitengo 4 ya mtedza umenewu, yomwe omugulitsayo anati ndi "Brazilian Nuts."
✓Koma kupyolera pa search yake pa makina a internate anapeza kuti mtedza uwu si Brazilian Nuts. Izi zimachitika pomwe mitengo yake inayamba kubereka.
✓Ndiye sanachedwe koma kufufuza ku Eden Green Nursery kuti kodi mtedza umenewu ndi wanji.
✓Ndipo ndinawatsikimizira kuti umenewu ndi "Malabar Chest nuts!"
✓Ndiye ananditsikimizira kuti tsiku lomwe alowe mu tawuni ya Lilongwe akatumiza; ndipo achitadi moteromo!
✓Kodi inuyo mukudziwa kuti kunja kuno kulinso mtedza umenewu?
✓Kodi mukudziwa kuti mtengo wa Malabar Chest nut ndi okongola zedi?
✓Nanga alipo pano ena omwe ali nawo?

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 06/07/2026

MPINIMBI, MDYANKHANDWE, MAHUHU, MTONONGOLI
✓Mainawo akutero
✓Zipatso zidetsa mano izi
✓Zimathandizira kupanga moyo wakumudzi kukhala okoma zedi.
✓Mitengo yake imapezeka m'tchire ndipo ndi yachilengedwe
✓Zipatsozi zikapya bwino zimayiyoka zokha mu mtengo ndipo timachita kutola pansi.
✓Timadya zaziwisi, kapena kuphika kapena zikhozanso kuumitsidwa kumene.
✓Zipatso izizi izi ndi zabwino zedi pa thanzi la munthu.
✓Kudako osakudabwa ayi ndi kuchurukidwa kwa ma "Anthocyanins."
✓Kumbukirani kuti ma "Anthocyanins" amateteza thupi Ku khansa, kutsitsa BP, kuteteza matenda a mtima komanso matenda a shuga.
✓Zirinsotu ndi mlingo waukuru wa vitamin A ndi vitamin C. Choncho limakuuza chitetezo cha matenda m'thupi komanso kuonjenzera thanzi labwino la maso.
✓Izo zirinso ndi B Vitamins monga Vitamin B1 ndi B6. Vitamin B6 amathandiza kuti mtima uzigunda moyenera.
✓Zirinso ndi michere monga Calcium, iron, potassium ndi zinc. Choncho ndiyofunikira pa thanzi labwino la mafupa.

Nthawi yakwana pomwe mitengo ngati iyi ikuguluka m'tchiremu, tiyambe kudzala mmakomo mwathu.

Osayiwala kuti akukupatsirani za thanzi patsamba lino ndi a Eden Green Nursery ku Ntcheu.
EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538.

05/07/2026

✓Chimanga Chofiira chikanalipobe
✓Mukafuna mbeu musakhale chete
✓Eden Green Nursery ku Ntcheu ikugulitsa ndithu pa mtengo wa k5000 per kg
✓Kumbukirani kuti ife a Eden Green Nursery ku Ntcheu tikukupatsirani za thanzi pa tsamba lino kupyolera mu thandizo lomwe timapeza mukatigula malonda omwe tikusatsa.

EDEN GREEN NURSERY IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 05/07/2026

UBWINO WA MASAMBA A MDYANKHANDWE (African Black Plum)
✓Ndapeza kuti mtengo umenewu ukudziwika ndi mayina awa:
1. Mpinimbi
2. Mahuhu
3. Mtonongoli
✓Masamba a mtengo umenewu akhoza kuphikidwa ndipo tiyi wakeyo akhoza kumwedwa makapu awiri patsiku kwa masiku osaposera 14.
✓Tiyi ameneyu akhoza kuthandiza anthu omwe:
1. Akudwala malungo kapena omwe akutentha thupi.
2. Anthu amene akutsegula mmimba
3. Anthu amene akutsegula mmimba mwa kamwanzi. Koma musanamwe kaoneneni ndi a dotolo kuti mudziwe kuti ndi chiyani chomwe chikupangitsa kuti mudzitsegula mmimba mwa kamwanzi.
5. Anthu amene akuvutika ndi likango.
6. Ndipo tiyiyo mukhoza kukhula pamalo pomwe palumikizana mafupa ngati pakuphwanya (arthritis)
7. Masamba ankhanda akhoza kupekesedwa mmanja mwaukhondo ndi kufinyira timadzi take mdiso ngati likupweteka limasiya.
8. Masamba a mtengowu akhoza kusinjidwa ndi kuika pa chironda. Amathandiza kuti chironda chipole mwachangu.

Mawa tiona kufunikira kwa makungwa a mtengo wa mpinimbi kapena kuti mahuhu!

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 05/07/2026

Kumudzi kwathu timati "Mdyankhandwe" sindikudziwa inu kuti zipatsozi mumazitcha kuti chiyani?

Ndizipatso zachilengedwe zopezeka m'tchire. Tikhala tikuona ubwino wake pa machiritso a matenda osiyana siyana!

02/07/2026

ANA A SUKURU TABWERANI PANO
✓Tikambirane pang'ono za kufunikira kwa chidede pakagwiridwe ntchito Ka ubongo komanso ntchito ya ubongo yosunga ndi kukumbukura zinthu.
✓Mwachidule chabe; ubongo uli ndi mbali ina yaing'ono yotchedwa kuti, "Hippocampus." Uku ndi komwe kumasindikizidwa komanso kusungidwa zinthu kwa kanthawi kochepa komanso nthawi yaitali.
✓Ndiye mbali imeneyi ikasokonekera munthu amatha kukumana ndi vuto la kusoweka chidwi pa zochitika, maphunziro, komanso kulemphera kukumbukira zinthu kumene. Akakhala mwana wasukuru ndiye kuti dziwani kuti zamvuta. Nzeru zimasoweka chifukwa sakhala ndi chidwi komanso satha kukumbuka zinthu.
✓Ndiyetu kumwa tiyi wa chidede kapu imodzi patsiku ndi kothandiza.
✓Chidede chiri ndi ma anthocyanins komanso ma polyphenols amene amateteza ubongo komanso kuulimbitsa kuti uzigwira bwino ntchito. Apa ndiye kuti Hippocampus amakhala kuti ali bwino komanso otetezeka ku "Oxidative stress."
✓Choncho ana asukulu atha kumamwa tiyi wa chidede, osati monga mankhwala, koma ngati chakumwa chopatsa ubongo thanzi labwino. Antha kumamwa mwa apo ndi apo; makapu awiri kapena atatu pa mlungu (masiku 7).

✓Ndiyetu ife a Eden Green Nursery tiri ndi chidede cha ufa (powder) chomwe tikugulitsa pa k6000 pa 200g.
✓Nambala ndi 0991183538
✓Tikupenzekera Ku Ntcheu pa Boma.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 01/07/2026

GONDOLOSI (African ginger)
✓Gondolosi ndi chimodzi mwa zomera zabwino zedi; komano mbiri yake inayipa kamba koti anthu amangoganiza zakuchipinda basi!
✓Ngakhale kuti Gondolosi ndi "aphrodisiac" wamphamvu kotero kuti amakuza libido mwa abambo ndi amayi omwe; iye ali ndi ubwino wina pa ubereki monga kuonjenzera chonde mwa abambo osabereka.
✓Gondolosi, sikuti tikuyang'anire kumbali ya kuchipinda kokha, koma ali ndi ntchito zina zochuruka.
✓Ali ndi vitamin D komanso Calcium yemwe ndi othandiza kuti mafupa akhale amphamvu. Amathandiza kuchiza matenda a mafupa kuphatikizapo kuziziritsa ululu wa pamalo polumikizanirana mafupa (arthritis)
✓Kuonjenzera apo Gondolosi ali ndi iron, zinc, copper, magnesium, vitamin A, komanso potassium ndi vitamin K.
✓Iye amaonjenzera mnyonga m'thupi
✓Amathandiza magazi kuti adziyenda bwino ndi kufikira mbali zonse za thupi.
✓Gondolosi amaphwanya, kusungunura ndi kuchotsa makhololo m'thupi. Izitu zikutanthauza kuti ali ndi kuthekera kothandiza asthma, chifuwa ndi chimfine. Ngakhale ana tikhoza kuwamwetsa gondolosi pa mlingo ochepa potengera ndi zaka komanso kulemera kwa matupi awo.
✓Anthu amene akuvutika ndi mavuto a mmimba; monga kusagaika bwino kwa chakudya, mpweya wammimba komanso kudzimbidwa akhoza kupeza bwino atamamwa tiyi wa gondolosi.
✓Ngakhale anthu amene akudwala mtundu wachiwiri wa nthenda ya shuga akhoza kuthandizika ndi gondolosi.
✓Gondolosi amatsitsa BP, amathandiza kuchiza matenda a mtima, komanso amakuza chitetezo cha matenda m'thupi.
✓Ali ndi ubwino waukuru pa thanzi labwino la ubongo ndipo amaonjenzera mnyonga za ubongo zokumbukira zinthu.

✓Koma gondolosi wabwino ndi yemwe mitsitsi yake yakhwima bwino ndipo makungwa okha ndi omwe agwiritsidwa ntchito.
✓Anthu ambiri amapanga gondolosi osachotsa makungwa; ndipo amaphatikiza makungwa ndi mitsitsi yomwe. Gondolosi uyu sakhala wamphamvu.
✓A Eden Green Nursery ku Ntcheu akupezeka ndi Gondolosi wabwino pa mtengo wa k6000 per 200 grams
0991183538.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 30/06/2026

CHIMANGA CHACHIKASU (NTHIKINYA)
✓Ichi ndi china mwa chimanga chopatsa thanzi.
✓Icho chiri ndi "Beta-caroteine, Lutein komanso Zeaxanthin."
✓Ndimakamba mobwereza-bwereza kuti tidzidya nsima ya kasintha sintha. Ndikutanthaiza ya chimanga chofiira, chachikasu, choyera komanso chakuda.
✓Zindikirani kuti chimanga chachikasu chiri ndi ma B vitamins monga Vitamin B3, B5, B6 ndi B9.
✓Vitamin B3 ndi ofunikira kwambiri pothana ndi vuto la kutentha kwa mapazi mwa anthu amene BP ndi yokwera.
✓Vitamin B6 amathandiza kuti mtima uzigunda moyenera.
✓Chimanga chimenechi chirinso ndi mlingo wabwino wa fiber, potassium, Calcium komanso zinc.
✓Choncho ichi ndi chimanga chomwe chimaonjenzera mnyonga m'thupi.
✓Chimalimbitsa mafupa, kuteteza khansa, matenda a shuga, matenda a mtima komanso matenda a maso, monga kuteteza ng'ala.
✓Chimathandiza kuthana ndi vuto la kudzimbidwa.

EDEN GREEN NURSERY IN NTCHEU
0991183538
✓Mukachifuna mutiuza chiripo ndipo ndi k3000 pa kg
✓Tikupezeka pa Ntcheu Boma.

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Ntcheu?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address


Ntcheu